ASILIKALI AKUFUNA KUPHA MTOLANKHANI GREGORY GONDWE

แชร์
ฝัง
  • เผยแพร่เมื่อ 10 ก.ย. 2024
  • ASILIKALI AWOPSEZA MTOLANKHANI GREGORY GONDWE
    Pano ali kobisala kuwopsa kumangidwa kapena kuphedwa
    Pa 29 January 2024, nyuzi yotsindikiza nkhani kudzera pa pa makina a internet ya Platform for Investigative Journalism (PIJ) inatulutsa nkhani ina imene ikuwulula za chinsinsi zimene boma la dziko lino lakhala likuchita ndi mkulu wina wa katangale amene amakhala mdziko la UK a Zunneth Sattar. Nkhaniyo imene inalembedwa ndi mkulu wa nyuzu yo a Gregory Gondwe inaloza chala ndikuwulula zonse zimene akulu akulu aku Mlawi Defense Force (MDF) akhala akuchita pomapanga migwirizano ndi munthu amene boma linalengeza kuti lasiya kuchita naye malonda. Kuwonjezera apo, nthambi ya Anti-Corruption Bureau (ACB) inalamula kuti nthambi ya MDF yi isachite malonda aliwonse azida za nkhondo ndi kamapni zilizonse za Sattar. Koma ayi, mwanseri nthambi ya MDF yakhala ikuchita malonda ndi mkuluyo mopanda manyazi.
    Pamene Platform for Investigative Journalism (PIJ) imatsindikiza nkhani yochititsa manyazi yi, nkuti nayo newspaper ya Daily Times inalembanso nkhani ngati yomweyi ndikuyika kutsogolo kwa nyuzi yawo (front page) ya tsiku limenelo pamene ndi pa 29 January 2024. Anayilemba nkhaniyi kumeneku ndi Mercy Matonga. Kutsatira kuwululika kuti boma mwanseri likupangabe za chinyengo ndi mkulu wa katangaleyu, anthu pamodzi ndi ma bungwe omenyera ufulu mdziko muno anakwiya nazo ndipo akufuna mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera awayankhule. Nafe pano pa Hanifa nkhaniyi tinakupatsirani tsatanatsatane wake pa 30 January 2024.
    Mukulemba kwake, Gregory Gondwe anawulula ndikutchula mayina akulu akulu aasilikali amene anapita ku Dubai mdziko la United Arab Emirates kukawona mmene galimoto zimene nthambi ya MDF yagula ku kampani ya a Malachite FZE ya a Sattar komwe kunalinso kukatsimikiza ngati ndi zomwe anagwirizana. Malingana ndi kalata imene anayisanira ndi Colonel Governor Gowa ndipo imapita kwa Ashok Nair amene ndi mnyamatawa a Sattar, anthu amene anapita nawo ku ulendo umenewu ndi monga a General Paul Valentino Phiri, Colonel Gilbert Mittawa, Colonel AE Simwaka, Lieutenant Colonel Thoko Chazema, Lieutenant Colonel KC Kadaluka, Captain Kennedy Nkhani ndi Warrant Officer Class II WO Mulenga

ความคิดเห็น • 49

  • @user-uc1pd1tc2x
    @user-uc1pd1tc2x 6 หลายเดือนก่อน +6

    Mai awawa ntchito amaigwira bwino zedi voice yake imachita Kukoma than Mr Hanifa

  • @greychizaka4088
    @greychizaka4088 6 หลายเดือนก่อน +3

    Long live Gregory Gondwe. Keepit up Hanifa

  • @JamusMigo-tk4mk
    @JamusMigo-tk4mk 6 หลายเดือนก่อน +5

    Thanks big boss

  • @augustMag
    @augustMag 6 หลายเดือนก่อน +1

    Mmmm Mr Gregory Tizikupemphererani kuti Mulungu akutetezeni pachili chonse Inuyo mumayima pa choona Ndipo Mulungu yekha ndi amene angakuthandizeni ngakhale mwana wa Mulungu adamupha kuti abise chona koma chifukwa CHOTI Mulungu anali naye chona sichinabisike pamene dziko likupephererani inunso muyime mmpemphero kunena zoonadi dziko la Malawi likusowa atola khani olimba mtima ngati inuyo Chauta akutetezeni kumene muli

  • @user-ez7th2rv7g
    @user-ez7th2rv7g 6 หลายเดือนก่อน +3

    God is watching 😮😮😮

  • @clintonhodda9830
    @clintonhodda9830 6 หลายเดือนก่อน +2

    Uchitsilu wa president chakwera mmalo mosintha akusaka munthu

  • @mackgozambia
    @mackgozambia 6 หลายเดือนก่อน +1

    Watching from KATETE Zambia

  • @kondwamlungu8384
    @kondwamlungu8384 6 หลายเดือนก่อน

    Ngati ziliko chonde MDF mukhululukileni Gregory Gondwe

  • @user-ce6hy6tp7e
    @user-ce6hy6tp7e 6 หลายเดือนก่อน +2

    Mcp ntchito zawo ndi zofuna kupha anthu amalawi munaziika pamoto

  • @lusolawo73
    @lusolawo73 6 หลายเดือนก่อน +2

    Best TV

  • @davidchirwa4683
    @davidchirwa4683 6 หลายเดือนก่อน +2

    mwachita bwino big man powulula zobisikazi

  • @user-zv3vw2hc6c
    @user-zv3vw2hc6c 6 หลายเดือนก่อน +1

    Koma Malawi amangoziwa kuzuza Anthu komaso kumpha ...koma kuthandiza anthu ayi 😢😢

  • @robertchikaonda-mu1bg
    @robertchikaonda-mu1bg 6 หลายเดือนก่อน +2

    MCP

  • @martinsailesi1731
    @martinsailesi1731 6 หลายเดือนก่อน

    Well done . Kuwelenga komveka bwino wosati zina zinja .

  • @user-ev6bi7jr7g
    @user-ev6bi7jr7g 6 หลายเดือนก่อน +3

    Ntchito za MCP ndi zimenezo kutereku MDF yo ili mkhwapa mwa MCP

  • @user-vf2fo1mb2c
    @user-vf2fo1mb2c 6 หลายเดือนก่อน

    May God protects us, Gondwe be free

  • @OustinYusuf
    @OustinYusuf 6 หลายเดือนก่อน

    Thanks very much ❤❤

  • @gladysbonongwe1038
    @gladysbonongwe1038 6 หลายเดือนก่อน +2

    Koma Aaaa dziko lathu laopsya

  • @BraveGadaffiMafayoNdlovu
    @BraveGadaffiMafayoNdlovu 6 หลายเดือนก่อน

    Tsinganene kut tsiku la 40 lidzakwana chifukwa calendar amathela pa 31 koma ndingonena kut 2025 akubwera mpamene chakwera adzadziwe kut ufa wa m'gayiwa ndi wa mapira wonse umaphika nsima koma uliwonse uli ndi anthu ake owukonda nthawi dzina madzi amayiwala khwawa nkutsekula lina khwawa

  • @felixharry3117
    @felixharry3117 6 หลายเดือนก่อน +1

    Mpaka dziko kumagula ndege za second hand kkkkk ndege za m'belo kkkk

  • @user-xm5bg9qi6b
    @user-xm5bg9qi6b 6 หลายเดือนก่อน

    Yehova akuona Gregory uli ngati Daniel mudzenje la mikango koma pompano kuyera

  • @mayesojameskatete
    @mayesojameskatete 6 หลายเดือนก่อน +1

    Thats MCP for you kupha anthu osisana nawo

    • @johnmpatama1461
      @johnmpatama1461 6 หลายเดือนก่อน

      Ntchito za Mcp ndi Kupha, Kuba, ndi Kuononga.

  • @user-tt3hq9lk7d
    @user-tt3hq9lk7d 6 หลายเดือนก่อน +1

    Nkhanizo ndizabodza nanu mli mdziko momuno koma simkudziwa zomwe zikuchitika dziko lokhala lanu

    • @dmankaymusic6730
      @dmankaymusic6730 6 หลายเดือนก่อน

      Aaaaaaa iwe ndiopusa eti zakhala lito zabodza ndiwe foreigner eti😂😂😂😂

    • @user-uc1pd1tc2x
      @user-uc1pd1tc2x 6 หลายเดือนก่อน

      Inu ndiachitsiru bwanji??? Aaaaaa kuputsa zedi umbuli Ndie wanu inu galu weniweni

    • @user-uc1pd1tc2x
      @user-uc1pd1tc2x 6 หลายเดือนก่อน

      ​@@dmankaymusic6730Ai ndiumbuki ndiachitsiru awaaaa brother asiyeni

    • @user-tt3hq9lk7d
      @user-tt3hq9lk7d 6 หลายเดือนก่อน

      Iwe nyini yamako wamva ukudziwa chani iweyo.

  • @tisuhmakhwah7085
    @tisuhmakhwah7085 6 หลายเดือนก่อน

    Camera muziika front kuti asamaoneke kut akuwelenga pena
    ..

  • @user-vl5on2lj8b
    @user-vl5on2lj8b 6 หลายเดือนก่อน

    Sopano inuyo akuboma makapha ntola nkhaniyu ndi zinthu zisika mitengo groceries magesi passport fuel asika ?

  • @InussaGoodson
    @InussaGoodson 6 หลายเดือนก่อน

    Samupeza cz ife tamusungatu

  • @AhmadumkomaTambala-lr9gp
    @AhmadumkomaTambala-lr9gp 6 หลายเดือนก่อน

    Koma MCP lazalo nzawo azisowa mtendele

  • @AleksaWilliams-qc6cn
    @AleksaWilliams-qc6cn 6 หลายเดือนก่อน

    Amuphelenji munthuyo, zaziii bas

  • @HopesonJailosi-vd6ou
    @HopesonJailosi-vd6ou 6 หลายเดือนก่อน

    Akanakhala kuti akuwanamizira sibwenzi ataopseza ntolankhaniyo

  • @WilfredMathews-yl6ij
    @WilfredMathews-yl6ij 6 หลายเดือนก่อน

    Anthu opusa awa

  • @user-cm4wk6td1d
    @user-cm4wk6td1d 6 หลายเดือนก่อน

    Koma zikoli eshiii

  • @SolomonNjolomole
    @SolomonNjolomole 6 หลายเดือนก่อน

    Achite manyazi a mdf akuululanibe tadziwa basi madzi atayika saolekanso .

  • @Rizikfarms
    @Rizikfarms 6 หลายเดือนก่อน +1

    Zamveka

  • @user-gt4sy5vz7i
    @user-gt4sy5vz7i 6 หลายเดือนก่อน

    MCP sopano 😢

  • @user-uc1pd1tc2x
    @user-uc1pd1tc2x 6 หลายเดือนก่อน

    MCP ndiye yokuphayo Komanso yokuba zedi agalu okhokha a MCP onse

  • @Moses51
    @Moses51 6 หลายเดือนก่อน

    Malawi wawola bc

  • @user-do2cs8nf4b
    @user-do2cs8nf4b 6 หลายเดือนก่อน

    Mulungu akutetezeren Paliponse mukuyenda

  • @Allieshaibu8612
    @Allieshaibu8612 6 หลายเดือนก่อน

    Usapha galu chakwera bwanji

  • @user-cb2cv9fz7m
    @user-cb2cv9fz7m 6 หลายเดือนก่อน

    Ameneyo samupha tu akunama zoonadi,adzibisalabe Bola choonadi tinacidziwa ndipo mwayaluka basi we always play for u brother be strong God his with u

  • @AmandaConstance-fx8cr
    @AmandaConstance-fx8cr 6 หลายเดือนก่อน

    Run 🏃‍♀️ 🏃‍♂️ for your life hide Mr

  • @actuarialscience2283
    @actuarialscience2283 6 หลายเดือนก่อน

    Kuti muyimvetsetse MCP mupite kukaona chinyawu.
    1) Chinyawu chimabisa nkhope yake momwemonso MCP imapanga katangale koma sifuna kuti anthu awulule.
    2) Chinyawu chimayitanitsa ndalama pamsewu moopseza koma ndalamayo siyipindulira amene waperekayo. MCP ikupanga zomwezo ndipo inayika ma tollgate awiri pa msewu umodzi. Koma msewo uli ndi ming'alu yokwanira 1 million. Instead of 1 million jobs we have 1 million potholes and 2 toll gates. Khalidwe la Chinyawu.
    3) Chinyawu chimapha momwemonso MCP imapha anthu.
    4) Chinyawu chimaba momwemonso MCP ndiyakuba
    Conclusion: Amalawi mukulamuliridwa ndi Satana=Chinyawu=MCP. Pamtumbo pake Chakwera.

    • @user-uc1pd1tc2x
      @user-uc1pd1tc2x 6 หลายเดือนก่อน

      Ndipo brother ukunena zoonad ndipo wafotokoza bwino zedi

  • @AlexKaunda-ny2eg
    @AlexKaunda-ny2eg 2 หลายเดือนก่อน

    Inuso asilikari musati bowe manyi anu mulibe chisoni ndi Amalawi