Ku Dowa Vote Ya Chakwera Kulibe Chifukwa A Chimwendo Ndi A Kawale Awononga Zinthu - Mzika Za Ku Dowa
ฝัง
- เผยแพร่เมื่อ 5 ก.พ. 2025
- On Nyasa VoiceBox, two Malawians from Dowa discuss how people in Dowa are unlikely to vote for President Chakwera and the Malawi Congress Party in the upcoming election. In their opinion, two Cabinet Ministers, Honorable Chimwendo Banda and Sam Kawale, are not performing their duties effectively. If the party hopes to win, these citizens urge the two ministers to change the way they work.
Pa Nyasa VoiceBox, Amalawi awiri aku Dowa akukambirana momwe anthu aku Dowa sangavotere a Chakwera komanso a Malawi Congress Party pachisankho chomwe chikubwerachi. M’malingaliro awo, nduna ziwiri za nduna za boma, Olemekezeka Chimwendo Banda ndi Sam Kawale, sakugwira ntchito yawo moyenera. Ngati chipanichi chikuyembekeza kupambana, nzikazi zipempha nduna ziwirizi kuti zisinthe momwe amagwirira ntchito.
#malawi
Hooooo! Koma yaaa! Ndale ku Nyasaland
Chirungamo ichi Big
Kodi ku dowa kuno tidzimvotela chikangawa chifukwa chani poti palibe chomwa wachita ndipo ndizooona kuti anthu amenewa ndiomwe awononga chipani.
Kuli konse kulibe AIP , pitani boma liri lonse its about only 20% to 17% thay has been accessed by farmers .
Mukunamizana ngati anthu aku Dowa amavotera MCP ili ku opposition ndiye Dowa ingasiye kuvotera MCP chifukwa mukunama ma cadet inu. Ku Thyolo poti amovoterabe DPP ngakhale nthawi ya Bingu mafuta ankavuta. Ulamuliriro wa Peter ngakhale unali osamva madandaulo aanthu monga kulembana ntchito potengera mtundu wa Chilomwe koma ku Thyolo anthu anavotera DPP mwaunyinji. Tisanamizanepo apa ndale zaku Malawi ndiza tsankho basi aliyense amati ndivotera president wa Chigawo chakwawo. Ndi pang'ono pokha anthu aku Mpoto amavotera munthu amene amuona kuti akuchita zabwino. Koma nawo amachita izi chifukwa chokakamizika chifukwa chigawo chawo chiri ndi anthu ochepa paokha sangatulutseko President ngakhale atakhala CANDIDATE yo kuti uyu akhoza kutithandiza apa ndiizi tingokakamira kumaimika azigogo mmaudindo a president chifukwa ndiochokera ku mmwera kapena pakati. Kuli achina Vitumbiko Mumba ndi Ntumbuka uku anyamata othamanga magazi tingowaonanga mmalo mowagwiritsa ntchito. Koma kufuna akuti pa speech yawo kumachita kuonjezera ma TWITTER kuti kapena anthu azimva zoyankhula zawo mawu anapita kalekale . Mtima ukufuna koma thupi likukana. A Malawi anatilodzayo ndiye analidi SIMBAZAKO weni weni.
Munthu uli pa area 3 ukulankhula zaku Dowa takudziwatu iwe
kho kho ,mawu opanda chigamba
Ine ndine mzika yakuno ku Dowa. Ndayenda mmadela ambiri kuno ku Dowa. Chikangawadi alibe vote Gyz. Anthu ndiwokwiya kwambiri. Chikangawa wautali ku Kasiya
Dowa , kuchipinda kwa chikangawa party
Zoona zake
😂😂😂😂 koma mumadziwa nchewa?
Inuyo musatinamize dowa singavotere winaso inuyo akupusitsani
Umbanda wayamba ndi chikangawa,tiyeni sipenye patali amalawi anzanga osazapanga mistake yovotera chikangawa komanso mp wina aliyense wachikangawa
Tingosintha mtsogoleri basi
Macadet awo inu, musatinyasepo apo
munyasidwa kumene simunati big
@@ChristopherManase-s1f ubwino wake nokha nokha Mulungu amaona si alomwe amenewo mukambran komko Chimwendo fertlizer wapereka kumwera uja za vote ayiwale
Mcp singangwe mukungwa ndinuyo
Komano mcp ya zunzadi anthu makosana
ulendo uno anthu achita moedzepeze , kapena tinene kuti kunyeledwa
Aku Dowa ndi anthunso amafuna ufa udzikhala mumtanga osati zofera kuti chipani chinabadwa kuno zimenezo ndizachikale anthu anasukusula panopa
Chimwendo ndi sam kawaleyo akusewera ndale zapamwamba, akupereka fertilizer ku mwera chifukwa akuti central region yonse ND kuchipinda kwawo
@geraldtuwaga-iz6ll Akumwerafe tapasidwa fertilizer chimanga koma za vote ayiwale nafeso kuno ndikuchipinda kwa DPP
MCP inayambira kumpoto amwene osanamizidwa Koma kuwapha Kuti atchuke akudowa kwanuko
Nonse mukusokosa apa ndinu a DPP mukuwonekelatu koma dziwani kuti or Chakwera atanyika motani solution siingakhale kupeleka vote kwamgogozi wanuyo osathekaaaa